Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 12:28-44 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

28. Atate, lemekezani dzina lanu. Pomwepo adadza mau ocokera Kumwamba, ndalilemekeza, ndipo ndidzalilemekezanso.

29. Cifukwa cace khamu la anthu akuimirirako, ndi kuwamva ananena kuti kwagunda. Ena ananena, Mngelo walankhula ndi iye.

30. Yesu anayankha nati, Mau awa sanafika cifukwa ca Ine, koma ca inu.

31. Tsopano pali kuweruza kwa dziko ili lapansi; mkulu wa dziko ili lapansi adzatayidwa kunja tsopano,

32. Ndipo Ine, m'mene ndikakwezedwa kudziko, ndidzakoka anthu onse kwa Ine ndekha.

33. Koma ananena ici ndi kuzindikiritsa imfa yanji akuti adzafa nayo.

34. Pamenepo khamulo linayankha iye, Tidamva ife m'cilamulo kuti Kristu akhala ku nthawi yonse; ndipo Inu munena bwanji, kuti Mwana wa munthu ayenera kukwezedwa? Mwana wa munthu amene ndani?

35. Pamenepo Yesu anati kwa iwo, Katsala kanthawi kakang'ono ndipo kuunika kuli mwa inu. 1 Yendani pokhala muli nako kuunika, kuti mdima sungakupezeni; ndipo woyenda mumdima sadziwa kumene amukako,

36. 2 Pokhala muli nako kuunika, khulupirirani kuunikako, kuti mukakhale ana a kuunikako.Izi Yesu analankhula, nacoka nawabisalira.

37. Koma angakhale adacita zizindikilo zambiri zotere pamaso pao iwo sanakhulupirira iye;

38. kuti mau a Yesaya mneneri akakwaniridwe, amene anati,3 Ambuye, wakhulupirira ndani kulalikira kwathu?Ndipo mkono wa Ambuye wabvumbulutsidwa kwa yani?

39. Cifukwa ca ici sanathe kukhulupira, pakuti Yesaya anatinso,

40. 4 Wadetsa maso ao, naumitsa mtima wao;Kuti angaone ndi maso, angazindikire ndi mtima,Nangatembenuke,Ndipo ndingawaciritse.

41. 5 Izi anati Yesaya, cifukwa anaona ulemerero wace; nalankhula za iye.

42. Kungakhale kotero, ambiri a mwa akuru anakhulupirira iye; koma 6 cifukwa ca Afarisi sanabvomereza, kuti angaletsedwe m'sunagoge,

43. 7 pakuti anakonda ulemerero wa anthu koposa ulemerero wa Mulungu.

44. Koma Yesu anapfuula nati, 8 iye wokhulupirira ine, sakhulupirira Ine, koma iye wondituma Ine.

Werengani mutu wathunthu Yohane 12