Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 10:1-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Iye wosalowa m'khola la nkhosa pakhomo, koma akwerera kwina, iyeyu ndiye wakuba ndi wolanda.

2. Koma iye wakulowera pakhomo, ndiye mbusa wa nkhosa.

3. Iyeyu, wapakhomo amtsegulira ndi nkhosa zimva mau ace; ndipo aitana nkhosa za iye yekha maina ao, nazitsogolera kunja.

4. Pamene adaturutsa zonse za iye yekha, azitsogolera; ndi nkhosa zimtsata iye; cifukwa zidziwa mau ace.

5. Koma mlendo sizidzamtsata, koma zidzamthawa; cifukwasizidziwa mau a alendo.

6. Fanizo ili Yesu ananena kwa iwo; koma sanazindikira zimene Yesu analikulankhula nao.

7. Cifukwa cace Yesuananenanso nao, Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Ine ndine khomo la nkhosa.

8. Onse amene anadza m'tsogolo mwa Ine ali akuba, ndi olanda: koma nkhosa sizinamva iwo.

9. Ine ndine khomo; ngati wina alowa ndi Ine, adzapulu-mutsidwa, nadzalowa, nadzaturuka, nadzapeza busa.

10. Siikudza mbala, koma kuti ikabe, ndi kupha, ndi kuononga, Ndadza Ine kuti akhale ndi moyo, ndi kukhala nao wocuruka.

11. Ine ndine Mbusa Wabwino; mbusa wabwino ataya moyo wace cifukwa ca nkhosa.

12. Wolipidwa amene sakhala mbusa, amene nkhosa siziri zace za yekha, aona mmbulu ulinkudza, nasiya nkhosazo, nathawa; ndipo mmbulu uzikwatula, nuzibalalitsa;

13. cifukwa ali wolipidwa, ndipo sasamala nkhosa.

14. Ine ndine Mbusa Wabwino; ndipo ndizindikira zanga, ndi zanga zindizindikira ine,

15. monga Atate andidziwa Ine, ndi Ine ndimdziwa Atate; ndipo nditaya moyo wanga cifukwa ca nkhosa.

16. Ndipo nkhosa zina ndiri nazo, zimene siziri za khola ili; izinso ndiyenera kuzitenga, ndipo zidzamva mau anga; ndipo zidzakhala gulu limodzi, mbusa mmodzi,

Werengani mutu wathunthu Yohane 10