Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 1:4-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Mwa iye munali moyo; ndi moyowu unali kuunika kwa anthu.

5. Ndipo kuunikaku kunawala mumdima; ndi mdimawu sunakuzindikira.

6. Kunali munthu, wotumidwa ndi Mulungu, dzina lace ndiye Yohane.

7. Iyeyu anadza mwa umboni kudzacita umboni za kuunikaku, kuti onse akakhulupirire mwa iye,

8. iye sindiye kuunikaku, koma anatumidwa kukacita umboni wa kuunikaku.

9. Uku ndiko kuunika kweni kweni, kumene kuunikira anthu onse akulowa m'dziko lapansi.

10. Anali m'dziko lapansi, ndi dziko linalengedwa ndi iye, koma dziko silinamzindikira iye.

11. Anadza kwa zace za iye yekha, ndipo ace a mwini yekha sanamlandira iye.

12. Koma onse amene anamlandira iye, kwa iwo anapatsa mphamvu yakukhala ana a Mulungu, kwa iwotu, akukhulupirira dzina lace;

13. amene sanabadwa ndi mwazi, kapena ndi cifuniro ca thupi, kapena ndi cifuniro ca munthu, koma ca Mulungu.

14. Ndipo Mau anasandulika thupi, nakhazikika pakati pa ife, ndipo tinaona ulemerero wace, ulemerero wonga wa wobadwa yekha wa Atate, wodzala ndi cisomo ndi coonadi.

15. Yohane acita umboni za iye, napfuula nati, Uyu ndiye amene ndinanena za iye, Wakudzayo pambuyo panga analipo ndisanabadwe ine; cifukwa anakhala woyamba wa ine.

16. Cifukwa mwa kudzala kwace tinalandira ife tonse, cisomo cosinthana ndi cisomo.

17. Cifukwa cilamulo cinapatsidwa mwa Mose; cisomo ndicoonadi zinadza mwa Yesu Kristu.

Werengani mutu wathunthu Yohane 1