Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 1:38-46 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

38. Koma Yesu anaceuka, napenya iwo alikumtsata, nanena nao, Mufuna ciani? Ndipo anati kwa iye, Rabi (ndiko kunena posandulika, Mphunzitsi), mukhala kuti?

39. Nanena nao, Tiyeni, mukaone, Pamenepo anadza naona kumene anakhala; nakhala ndi iye tsiku lomwelo; panali monga ora lakhumi.

40. Andreya mbale wace wa Simoni Petro anali mmodzi wa awiriwo, anamva Yohane, namtsata iye.

41. Anayamba iye kupeza mbale wace yekha Simoni, nanena naye, Tapeza ife Mesiya (ndiko kusandulika Kristu).

42. Anadza naye kwa Yesu. M'mene anamyang'ana iye, anati, Uli Simoni mwana wa Yohane; 11 udzachedwa Kefa (ndiko kusandulika Petro).

43. M'mawa mwace anafuna kuturuka kunka ku Galileya, napeza Filipo, Ndipo Yesu ananena naye, Tsata Ine.

44. Koma Filipo anali wa ku Betsaida, mudzi wa Andreya ndi Petro.

45. Filipo anapeza Natanayeli, nanena naye, iye 12 amene Mose analembera za iye m'cilamulo, ndi aneneri, tampeza, ndiye Yesu mwana wa Yosefe wa ku Nazarete.

46. Natanayeli anati kwa iye, 13 Ku Nazarete nkutha kucokera kanthu kabwino kodi? Filipo ananena naye, Tiye ukaone.

Werengani mutu wathunthu Yohane 1