Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 1:16-29 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Cifukwa mwa kudzala kwace tinalandira ife tonse, cisomo cosinthana ndi cisomo.

17. Cifukwa cilamulo cinapatsidwa mwa Mose; cisomo ndicoonadi zinadza mwa Yesu Kristu.

18. Kulibe munthu anaona Mulungu nthawi zonse; Mwana wobadwa yekha wakukhala pa cifuwa ca Atate, Iyeyu anafotokozera.

19. Ndipo umene ndiwo umboni wa Yohane, pamene Ayudaanatuma kwa iye ansembe ndi alembi a ku Yerusalemu akamfunse iye, Ndiwe yani?

20. Ndipo anabvomera, wosakana; nalola kuti, Sindine Kristu.

21. Ndipo anamfunsa iye, Nanga bwanji? ndiwe Eliya kodi? Nanena iye, Sindine iye, Ndiwe Mneneriyo kodi? Nayankha, Iai.

22. Cifukwa cace anati kwa iye, Ndiwe yani? kuti tibwezere mau kwa iwo anatituma ife. Unena ciani za iwe wekha?

23. Anati, 1 Ndine mau a wopfuula m'cipululu, Lungamitsani njira ya Mbuye, monga anati Yesaya mneneriyo.

24. Ndipo otumidwawo analia kwa Marisi.

25. Ndipo anamfunsa iye, nati kwa iye, Koma ubatiza bwanji, ngati suli Kristu, kapena Eliya, kapena Mneneriyo?

26. Yohane anawayankha, nati, 2 Ine ndibatiza ndi madzi; pakati pa inu paimirira amene simumdziwa,

27. 3 ndiye wakudza pambuyo panga, amene sindiyenera kummasulira lamba la nsapato yace.

28. Zinthu izi zinacitika m'Betaniya tsidya lija la Y ordano, pomwe analikubatiza Yohane.

29. M'mawa mwace anaona Yesu alinkudza kwa iye, nanena, 4 Onani Mwanawankhosa wa Mulungu 5 amene acotsa cimo lace la dziko lapasi!

Werengani mutu wathunthu Yohane 1