Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yakobo 5:11-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Taonani tiwayesera odala opirirawo; mudamva za cipiriro ca Yobu, ndipo mwaona citsiriziro ca Ambuye, kuti Ambuye ali wodzala cikondi, ndi wacifundo.

12. Koma makamaka, abale anga, musalumbire, kungakhale kuchula mwamba kapena dziko, kapena lumbiro lina liri lonse; koma inde wanu akhale inde, ndi iai wanu akha; le iai; kuti mungagwe m'ciweruziro.

13. Kodi wina wa inu akumva zowawa? Apemphere, Kodi wina asekera? Ayimbire.

14. Pali wina kodi adwala mwa inu? Adziitanire akuru a Mpingo, ndipo apemphere pa iye, atamdzoza ndi mafuta m'dzina la Ambuye:

15. ndipo pemphero la cikhulupiriro lidzapulumutsa wodwalayo, ndipo Ambuye adzamuukitsa; ndipo ngati adacita macimo adzakhululukidwa kwa iye.

16. Cifukwa cace mubvomerezane wina ndi mnzace macimo anu, ndipo mupempherere wina kwa mnzace kuti muciritsidwe. Pemphero la munthu wolungama likhoza kwakukuru m'macitidweace.

17. Eliya anali munthu wakumva zomwezi tizimva ife, ndipo anapemphera cipempherere kuti isabvumbe mvula; ndipo, siinagwa mvula pa dzikozaka zitatu kudza miyezi isanu ndi umodzi.

18. Ndipo anapempheranso; ndipo m'mwamba munatsika mvula, ndi dziko lidabala zipatso zace.

19. Abale anga, ngati wina wa inu asocera posiyana ndi coonadi, ndipo ambweza iye mnzace;

20. azindikire, kuti iyeamene abweza wocimwa ku njira yace yosocera adzapulumutsa munthu kwa imfa, ndipo adzabvundikira macimo aunyinji.

Werengani mutu wathunthu Yakobo 5