Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yakobo 2:19-26 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

19. Ukhulupirira iwe kuti Mulungu ali mmodzi; ucita bwino; ziwanda zikhulupiranso, ndipo zinthunthumira.

20. Koma ufuna kuzindikira kodi, munthu wopanda pace iwe, kuti cikhulupiriro copanda nchito ciri cabe?

21. Abrabamu kholo lathu, sanayesedwa wolungama ndi nchito kodi, paja adapereka mwana wace Isake nsembe pa guwa la nsembe?

22. Upenya kuti cikhulupiriro cidacita pamodzi ndi nchito zace, ndipo moturuka mwa nchito cikhulupiriro cidayesedwa cangwiro;

23. ndipo anakwaniridwa malembo onenawa, Ndipo Abrahamu anakhulupirira Mulungu, ndipo kudawerengedwa kwa iye cilungamo; ndipo anachedwa bwenzi la Mulungu.

24. Mupenya kuti munthu ayesedwa wolungama ndi nchito yace, osati ndi cikhulupiriro cokha.

25. Ndipo momwemonso sanayesedwa wolungama Rahabi mkazi wa damayo ndi nchito kodi, popeza adalandira amithenga, nawaturutsa adzere njira yina?

26. Pakuti monga thupi lopanda mzimu liri lakufa, koteronso cikhulupiriro copanda nchito ciri cakufa.

Werengani mutu wathunthu Yakobo 2