Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yakobo 2:14-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Cipindulocace nciani, abale anga, munthu akanena, Ndiri naco cikhulupiriro, koma alibe nchito? Kodi cikhulupiriroco cikhoza kumpulumutsa?

15. Mbale kapena mlongo akakbalawausiwa, nieikamsowa cakudya ca tsiku lace,

16. ndipo wina wa inu akanena nao, Mukani ndi mtendere, muitapfunde ndi kukhuta; osawapatsa iwo zosowa za pathupi; kupindula kwace nciani?

17. Momwemonso cikhulupiriro, cikapanda kukhala nazo nchito, cikhala cakufa m'kati mwacemo.

18. Koma wina akati, Iwe uli naco cikhulupiriro, ndipo ine ndiri nazo nchito; undionetse ine cikhulupiriro cako copanda nchito zako, ndipo ine ndidzakuonetsa iweeikhulupiriro canga coturuka m'nchito zanga.

19. Ukhulupirira iwe kuti Mulungu ali mmodzi; ucita bwino; ziwanda zikhulupiranso, ndipo zinthunthumira.

20. Koma ufuna kuzindikira kodi, munthu wopanda pace iwe, kuti cikhulupiriro copanda nchito ciri cabe?

Werengani mutu wathunthu Yakobo 2