Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yakobo 1:6-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Koma apemphe ndi cikhulupiriro, wosakayika konse; pakuti wokayikayo afanana ndi pfunde la nyanja lotengeka ndi mphepo ndi kuwinduka nayo.

7. Pakuti asayese munthu uyu kuti adzalandira kanthu kwa Ambuye;

8. munthu wa mitima iwiri akhala wosinkhasinkha pa njira zace zonse.

9. Koma mbale woluluka adzitamandire pa ukulu wace;

10. pakuti adzapita monga duwa la udzu,

11. Pakuti laturuka dzuwa ndi kutentha kwace, ndipo laumitsa udzu; ndipo lathothoka duwa lace, ndi ukoma wa maonekedwe ace waonongeka; koteronso wacuma adzafota m'mayendedwe ace.

12. Wodala munthu wakupirira poyesedwa; pakuti pamene wabvomerezeka, adzalandira korona wa moyo, amene Ambuye adalonjezera iwo akumkonda iye.

13. Munthu poyesedwa, asanena, Ndiyesedwa ndi Mulungu; pakuti Mulungu sakhoza kuyesedwa ndi zoipa, ndipo iye mwini sayesa munthu:

14. koma munthu ali yense ayesedwa pamene cilakolako cace ca iye mwini cimkokera, nicimnyenga.

15. Pamenepo cilakolakoco citaima, cibala ucimo; ndipo ucimo, utakula msinkhu, ubala imfa.

16. Musanyengedwe, abale anga okondedwa.

17. Mphatso iri yonse yabwino, ndi cininkho ciri conse cangwiro zicokera Kumwamba, zotsika kwa Atate wa mauniko, amene alibe cisanduliko, kapena mthunzi wa citembenukiro.

18. Mwa cifuniro cace mwini anatibala ife ndi mau a coonadi, kuti tikhale ife ngati zipatso zoundukula za zolengedwa zace.

19. Mudziwa, abale anga okondedwa, kuti munthu ali yense akhale wochera khutu, wodekha polankhula, wodekha pakupsa mtima.

20. Pakuti mkwiyo wa munthu sucita cilungamo ca Mulungu.

21. Mwa ici, mutabvula cinyanso conse ndi cisefukiro ca coipa, landirani ndi cifatso mau ookedwa mwa inu, okhoza kupulumutsa moyo wanu.

Werengani mutu wathunthu Yakobo 1