Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yakobo 1:24-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

24. pakuti wadziyang'anira yekha nacoka, naiwala pompaja nali wotani.

25. Koma iye wakupenyerera m'lamulo langwiro, ndilo laufulu, natero cipenyerere, ameneyo, posakhala wakumva wakuiwala, komatu wakucita nchito, adzakhala wodala m'kucita kwace.

26. Ngati wina adziyesera ali wopembedza Mulungu, ndiye wosamanga lilime lace, koma adzinyenga mtima wace, kupembedza kwace kwa munthuyu nkopanda pace.

27. Mapembedzedwe oyera ndi osadetsa pamaso pa Mulungu ndi Atate ndiwo: z kuceza ndi ana amasiye ndi akazi amasiye m'cisautso cao, ndi 1 kudzisungira mwini wosacitidwa mawanga ndi dziko lapansi.

Werengani mutu wathunthu Yakobo 1