Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Tito 1:8-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. komatu wokonda kucereza alendo, wokonda zokoma, wodziweruza, wolungama, woyera mtima, wodziletsa;

9. wogwira mau okhulupirika monga mwa ciphunzitso, kuti akakhoze kucenjeza m'ciphunzitso colamitsa, ndi kutsutsa otsutsana naye.

10. Pakuti alipo ambiri osamvera mau, olankhula zopanda pace, ndi onyenga, makamaka iwo a kumdulidwe,

11. amene ayenera kutsekedwa pakamwa; ndiwo amene apasula mabanja banja lonse, ndi kuphunzitsa zosayenera cifukwa ca cisiriro conyansa.

12. Wina wa mwa iwo, ndiye mneneri wa iwo okha, anati, Akrete ndiwo amabodza masiku onse, zirombo zoipa, aumbombo, aulesi.

13. Umboni uwu uli woona. Mwa ici uwadzudzule mokaripa, kuti akakhale olama m'cikhulupiriro,

14. osasamala nthanu zacabe za Ciyuda, ndi malamulo a anthu opatuka kusiyana naco coonadi.

15. Zonse ziyera kwa iwo amene ayera mtima; koma kwa iwo odetsedwa ndi osakhulupira kulibe kanthu koyera; komatu zadetsedwa nzeru zao ndi cikumbu mtima cao.

16. Abvomereza kuti adziwa Mulungu, koma ndi Debito zao amkana iye, popeza ali onyansitsa, ndi osamvera, ndi pa nchito zonse zabwino osatsimikizidwa.

Werengani mutu wathunthu Tito 1