Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Marko 9:33-44 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

33. Ndipo iwo anadza ku Kapernao; ndipo pamene anakhala m'nyumba, Iye anawafunsa, Munalikutsutsana ninji panjira?

34. Koma iwo anakhala cete; pakuti anatsutsana wina ndi mnzace panjira, kuti, wamkuru ndani?

35. Ndipo m'mene anakhala pansi anaitana khumi ndi awiriwo; nanena nao, Ngati munthu afuna kukhala woyamba, akhale wakuthungo wa onse, ndi mtumiki wa onse.

36. Ndipo anatenga kamwana, nakaika pakati pao, nakayangata, nanena nao,

37. Munthu ali yense adzalandira kamodzi ka tiana totere cifukwa ca dzina langa, alandira ine; ndipo yense amene akalandira Ine, salandira Ine, koma Iye amene anandituma Ine.

38. Yohane anati kwa Iye, Mphunzitsi, tinaona munthu alikuturutsa ziwanda m'dzina lanu; ndipo tinamletsa, cifukwa sanalikutsata ife.

39. Koma Yesu anati, Musamamletsa iye; pakuti palibe munthu adzacita camphamvu m'dzina langa, nadzakhoza msanga kundinenera Ine zoipa.

40. Pakuti iye wosatsutsana ndi ife athandizana nafe.

41. Pakuti munthu ali yense adzakumwetsani inu cikho ca madzi m'dzina langa cifukwa muli ace a Kristu, indetu ndinena ndi inu, kuti iye sadzataya konse mphotho yace.

42. Ndipo yense amene adzalakwitsa kamodzi ka tiana timeneto takukhulupirira Ine, kuli kwabwino kwa iye makamaka kuti mwala waukuru wamphero ukolowekedwe m'khosi mwace, naponyedwe iye m'nyanja.

43. Ndipo ngati dzanja lako likulakwitsa iwe, ulidule: nkwabwino kwa iwe kulowa m'moyo wopunduka dzanja, koposa kukhala ndi manja ako awiri ndi kulowa m'gehena, m'moto wosazima.[

44. ]

Werengani mutu wathunthu Marko 9