Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Marko 9:1-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo ananena nao, Ndithu ndinena ndi inu kuti, Alipo ena akuimirira pano, amene sadzalawa imfa konse, kufikira akaona Ufumu wa Mulungu utadza ndi mphamvu.

2. Ndipo atapita masiku asanu ndi limodzi, Yesu anatenga Petro, ndi Yakobo, ndi Yohane, nakwera nao pa phiri lalitali padera pa okha; ndipo anasandulika pamaso pao:

3. ndipo zobvala zace zinakhala zonyezimira, zoyera mbu; monga ngati muomba wotsuka nsaru pa dziko lapansi sangathe kuziyeretsai.

4. Ndipo anaonekera kwa iwo Eliya ndi Mose, alikulankhulana ndi Yesu.

5. Ndipo Petro anayankha, nanena ndi Yesu, Rabi, kutikomera ife kukhala pano; ndipo timange misasa itatu; umodzi wa inu, ndi wina wa Mose, ndi wina wa Eliya.

6. Pakuti sanadziwa cimene adzayankha; cifukwa anacita mantha ndithu.

7. Ndipo panadza mtambo wakuwaphimba iwo; ndipo mau munaturuka m'mtambomo, kuti, Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa; mverani Iye.

8. Ndipo dzidzidzi pounguzaunguza, sanapenya munthu wina yense, koma Yesu yekha, ndi iwo eni.

Werengani mutu wathunthu Marko 9