Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Marko 8:7-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Ndipo anali nato tinsomba towerengeka; ndipo Iye anatidalitsa, nati atipereke itonso.

8. Ndipo anadya nakhuta; ndipo anatola makombo malicero asanu ndi awiri.

9. Ndipo iwo anali ngati zikwi zinai; ndipo Iye analawirana nao.

10. Ndipo pomwepo analowa m'ngaiawa ndi akhupunzira ace, nafika ku mbali ya ku Dalmanuta.

11. Ndipo Afarisi anaturuka, nayamba kufunsana naye, ndi kufuna kwa Iye cizindikilo cocokera Kumwamba, namuyesa Iye.

12. Ndipo anausitsa moyo m'mzimu wace, nanena, Anthu a mbadwo uno afunafuna cizindikilo bwanji? indetu ndinena kwa inu, ngati cizindikilo cidzapatsidwa kwa mbadwo uno!

13. Ndipo anawasiya iwo, nalowanso m'ngalawa, nacoka kunka ku tsidya lija.

14. Ndipo ophunzira adaiwala kutenga mikate, ndipo analibe mkate m'ngalawa koma umodzi wokha.

15. Ndipo Iye anawalamula, nanena, Yang'anirani, penyani kuti mupewe cotupitsa mkate ca Afarisi, ndi cotupitsa mkate ca Herode.

16. Ndipo anatsutsana wina ndi mnzace, nanena kuti, Tiribe mikate.

17. Ndipo Yesu pamene anazindikira, ananena nao, Bwanji mutsutsana cifukwa mulibe mkate? kodi kufikira tsopano simuzindikira, nisimudziwitsa? kodi muli nayo mitima yanu youma?

18. Pokhala nao maso simupenya kodi? ndi pokhala nao makutu simukumva kodi? ndipo simukumbukila kodi?

19. Pamene ndinawagawira anthu zikwi zisanu mikate isanu ija, munatola mitanga ingati yodzala ndi makombo? Ananena naye, Khumi ndi iwiri.

20. Ndipo mikate isanu ndi iwiri kwa anthu zikwi zinai, munatola malicero angati odzala ndi makombo? Ndipo ananena naye, Asanu ndi awiri.

21. Ndipo Iye ananena nao, Simudziwitsa ngakhale tsopano kodi?

22. Ndipo anadza ku Betsaida. Ndipo anadza naye kwa Iye munthu wakhungu, nampempha Iye kuti amkhudze.

23. Ndipo anamgwira dzanja munthu wakhunguyo, naturukira naye kunja kwa mudzi; ndipo atamthira malobvu m'maso mwace, naika manja pa iye, anamfunsa, Uona kanthu kodi?

Werengani mutu wathunthu Marko 8