Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Marko 2:20-28 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

20. Koma adzadza masiku, pamene mkwati adzacotsedwa kwa iwo, ndipo pamenepo adzasala kudya tsiku lomwelo.

21. Palibe munthu asokerera cigamba ca nsaru yaiwisi pa copfunda cakale; pena cimene coti cidzakonza cizomolapo, catsopanoco cizomoka pa cakaleco, ndipo ciboo cikulapo.

22. Ndipo palibe munthu amatsanulira vinyo watsopano m'matumba akale: pena vinyo adzaphulitsa matumba, ndipo aonongeka vinyo, ndi matumba omwe: koma vinyo watsopano amatsanulira m'matumba atsopano.

23. Ndipo kunali kuti anapita Iye pakati pa minda dzuwa la Sabata; ndipo ophunzira ace poyenda anayamba kubudula ngala za dzinthu.

24. Ndipo Afarisi ananena ndi Iye, Taona, acitiranji cosaloleka kucitika dzuwa la Sabata?

25. Ndipo ananena nao, Simunawerenga konse cimene anacicita Davide, pamene adasowa, namva njala, iye ndi iwo amene anali pamodzi naye?

26. Kuti, analowa m'nyumba ya Mulungu masiku a Abyatara, mkulu wa ansembe, ndipo anadya mikate yoonetsera, yosaloleka kudya ena, koma ansembe okha, ndipo anawapatsanso iwo amene anali naye?

27. Ndipo ananena nao, Sabata linaikidwa cifukwa ca munthu, si munthu cifukwa ca Sabata;

28. motero Mwana wa munthu ali mwini dzuwa la Sabata lomwe.

Werengani mutu wathunthu Marko 2