Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Marko 2:1-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo polowanso Iye m'Kapernao atapita masiku ena, kunamveka kuti ali m'nyumba.

2. Ndipo ambiri anaunjikana, kotero kuti anasowa malo, ngakhale pakhomo pomwe; ndipo analankhula nao mau.

3. Ndipo anadza kwa Iye otenga munthu wodwala manjenje, wonyamulidwa ndi anthu anai.

4. Ndipo pamene sanakhoza kufika kuli Iye, cifukwa ca khamu la anthu, anasasula chindwi pokhala Iye; ndipo pamene anatha kuliboola, anatsitsa mphasa m'mene alinkugonamo wodwala manjenjeyo,

5. Ndipo Yesu pakuona cikhulupiriro cao ananena ndi wodwala manjenje, Mwana, macimo ako akhululukidwa.

6. Koma anakhalapo ena a alembi akuganizira mumtima mwao,

7. Munthu amene atero bwanji? acita mwano; akhoza ndani kukhululukira macimo, koma mmodzi, ndiye Mulungu?

Werengani mutu wathunthu Marko 2