Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Marko 16:10-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Iyeyu anapita kuwauza iwo amene adafokhala naye, ali ndi cisoni ndi kulira misozi.

11. Ndipo iwowo, pamene anamva kuti ali moyo, ndi kuti adapenyeka kwa iye, sanamvera.

12. Ndipo zitatha izi, anaonekanso Iye m'maonekedwe ena kwa awiri a iwo alikuyenda kupita kumiraga,

13. Ndipo iwowa anacoka nawauza otsala; koma iwo omwe sanawabvomereza.

14. Ndipo citatha ico anaonekera kwa khumi ndi mmodzi iwo okha, alikuseama pacakudya; ndipo anawadzudzula cifukwa ca kusabvomereza kwao ndi kuuma mtima, popeza sanabvomereza iwo amene adamuona, atauka Iye.

15. Ndipo ananena nao, mukani ku dziko lonse lapansi, lalikirani Uthenga Wabwino kwa olengedwa onse.

16. Amene akhulupirira nabatizidwa, adzapulumutsidwa; koma amene sakhulupirira adzalangidwa.

17. Ndipo zizindikilo izi zidzawatsata iwo akukhulupirira; m'dzina langa adzaturutsa ziwanda; adzalankhula ndi malankhulidwe atsopano;

18. adzatola njoka, ndipo ngakhale akamwa kanthu kakufa nako, sikadzawapweteka; adzaika manja ao pa odwala, ndipo adzacira.

Werengani mutu wathunthu Marko 16