Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Marko 16:1-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo litapita Sabata, Maliya wa Magadala, ndi Maliya amace wa Yakobo, ndi Salome, anagula zonunkhira, kuti akadze kumdzoza Iye.

2. Ndipo anadza kumanda mamawa tsiku loyamba la Sabata, litaturuka dzuwa.

3. Ndipo analikunena mwa okha, Adzatikunkhunizira ndam mwalawo, pa khomo la manda?

4. Ndipo pamene anakweza maso anaona kuti mwala wakunkhunizidwa pakuti unali waukuru ndithu.

5. Ndipo pamene analowa m'manda, anaona mnyamata alikukhala ku mba li va ku dzanja lamanja, wobvala mwinjiro woyera; ndipo iwo anadabwa.

6. Ndipo iye ananena nao, Musadabwe: mulikufuna Yesu Mnazarene amene anapacikidwa: anauka; sali pano; taonani, mbuto m'men e anaikamo Iye!

7. Koma mukani, uzani ophunzira ace, ndi Petro, kuti akutsogolerani inu ku Galileya; kumeneko mudzamuona Iye, monga ananena ndi inu.

Werengani mutu wathunthu Marko 16