Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Marko 14:55-72 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

55. Ndipo ansembe akuru ndi akuru a milandu onse anafunafuna umboni wakutsutsa nao Yesu kuti amuphe Iye; koma sanaupeza.

56. Pakuti ambiri anamcitira umboni wonama, ndipo umboni wao sunalingana.

57. Ndipo ananyamukapo ena, namcitira umboni wakunama, nanena kuti,

58. Ife tinamva Iye alikunena, kuti, Ine ndidzaononga Kacisi uyu wopangidwa ndi manja, ndi masiku atatu ndidzamanga wina wosapangidwa ndi manja.

59. Ndipo ngakhale momwemo umboni wao sunalingana.

60. Ndipo mkulu wa ansembe ananyamuka pakati, namfunsa Yesu, nanena, Suyankha kanthu kodi? Nciani ici cimene awa alikucitira mboni?

61. Koma anakhala cete, osayankhakanthu. Mkulu wa ansembe anamfunsanso, nanena naye, Kodi Iwe ndiwe Kristu, Mwana wace wa Wolemekezeka?

62. Ndipo Yesu anati, Ndine amene; ndipo mudzaona Mwana wa munthu alikukhala ku dzanja lamanja la mphamvu, ndi kudza ndi mitambo ya kumwamba.

63. Ndipo mkulu wa ansembe anang'amba maraya ace, nanena, Tifuniranjinso mboni zina?

64. Mwamva mwano wace; muyesa bwanji? Ndipo onse anamtsutsa Iye kuti ayenera kufa.

65. Ndipo ena mayamba kumthira malobvu Iye, adi kuphimba nkhope yace, ndi cumbwanyula, ndi kunena naye, Lota; ndipo anyamatawo ananpanda Iye kofu.

66. Ndipo pamene Petro anali iansi m'bwalo, anadzapo mmodzi va adzakazi a mkulu wa ansembe;

67. ndipo anaona Petro alikuotha noto, namyang'ana iye, nanena, wenso unali naye Mnazarene, Yesu.

68. Koma anakana, nanena, Sindidziwa kapena kumvetsa cimene ucinena iwe; ndipo anaturuka kunka kucipata; ndipo tambala analira.

69. Ndipo anamuona mdzakaziyo, nayambanso kunena ndi iwo akuimirirapo, Uyu ngwa awo.

70. Koma anakananso. Ndipo patapita kamphindi, akuimirirapo ananenanso ndi Petro, Zedi uli wa awo; pakutinso uti Mgalileya.

71. Koma iye anayamba kutemberera, ndi kulumbira, Sindimdziwa munthuyu mulikunena.

72. Ndipo pomwepo tambala analira kaciwiri. Ndipo Petro anakumbukila umo Yesu anati kwa iye, kuti, Tambala asanalire kawiri udzandikana katatu. Ndipo pakuganizira ici analira misozi.

Werengani mutu wathunthu Marko 14