Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Marko 14:44-55 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

44. Ndipo wakumpereka Iye anawapatsa cizindikilo, nanena, Iye amene ndidzampsompsona, ndiyetu; mgwireni munke naye cisungire.

45. Ndipo atafika, pomwepo anadza kwa Iye, nanena, Rabi; nampsompsonetsa.

46. Ndipo anamthira manja, namgwira.

47. Koma mmodzi wina wa iwo akuimirirapo, anasolola lupanga lace, nakantha kapolo wace wa mkulu wa ansembe, namdula khutu lace.

48. Ndipo Yesu anayankha nati kwa iwo, Kodi mwaturuka ndi malupanga ndi mikunkhu kundigwira ine monga wacifwamba?

49. Masiku onse ndinali nanu m'Kacisi ndirikuphunzitsa, ndipo simunandigwira Ine; koma ici cacitika kuti malembo akwanitsidwe.

50. Ndipo iwo onse anamsiya Iye, nathawa.

51. Ndipo mnyamata wina anamtsata Iye, atapfundira pathupi bafuta yekha; ndipo anamgwira;

52. koma iye anasiya bafutayo, nathawa wamarisece.

53. Ndipo ananka naye Yesu kwa mkulu wa ansembe; ndipo anasonkhana kwa iye ansembe akuru onse ndi akuru a anthu, ndi alembi,

54. Ndipo Petro adamtsata Iye kutali, kufikira kulowa m'bwalo la mkulu wa ansembe; ndipo anali kukhala pansi pamodzi ndi anyamata, ndi kuotha moto.

55. Ndipo ansembe akuru ndi akuru a milandu onse anafunafuna umboni wakutsutsa nao Yesu kuti amuphe Iye; koma sanaupeza.

Werengani mutu wathunthu Marko 14