Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Marko 14:39-48 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

39. Ndipo anacokanso, napemphera, nanena mau omwewo.

40. Ndipo anadzanso nawapeza ali m'tulo, pakuti maso ao analemeradi; ndipo sanadziwa comyankha Iye.

41. Ndipo anadza kacitatu, nanena nao, Gonani tsopano, nimupumule; cakwanira; yafika nthawi; onani Mwana wa munthu aperekedwa m'manja a anthu ocimwa.

42. Ukani, tizimuka; onani wakundiperekayo ali pafupi.

43. Ndipo pomwepo, Iye ali cilankhulire, anadza Yudase, mmodzi wa khumi ndi awiriwo, ndipo pamodzi naye khamu la anthu, ali nao malupanga ndi mikunkhu, ocokera kwa ansembe akuru ndi alembi ndi akuru.

44. Ndipo wakumpereka Iye anawapatsa cizindikilo, nanena, Iye amene ndidzampsompsona, ndiyetu; mgwireni munke naye cisungire.

45. Ndipo atafika, pomwepo anadza kwa Iye, nanena, Rabi; nampsompsonetsa.

46. Ndipo anamthira manja, namgwira.

47. Koma mmodzi wina wa iwo akuimirirapo, anasolola lupanga lace, nakantha kapolo wace wa mkulu wa ansembe, namdula khutu lace.

48. Ndipo Yesu anayankha nati kwa iwo, Kodi mwaturuka ndi malupanga ndi mikunkhu kundigwira ine monga wacifwamba?

Werengani mutu wathunthu Marko 14