7. Ndipo m'mene mudzamva za nkhondo ndi mbiri zace za nkhondo, musamadera nkhawa: ziyenerakucitika izi; koma sicinafike cimariziro.
8. Pakuti mtundu wa anthu udzayambana ndi mtundu wina, ndipo ufumu ndi ufumu unzace: padzakhaia zibvomezi m'malo m'malo; padzakhala njala; izi ndi zoyambira za zowawa.
9. Koma inu mudziyang'anire inu nokha; pakuti adzakuperekani inu kwa akuru a mirandu; ndipo adzakukwapulani m'masunagoge; ndipo pamaso pa akazembe ndi mafwnu mudzaimirira cifukwa ca Ine, kukhale umboni kwa iwo.
10. Ndipo Uthenga Wabwino uyenera uyambe kulalikidwa kwa anthu a mitundu yonse.
11. Ndipo pamene adzapita nanu kumlandu, nadzakuperekani, musada nkhawa usanayambe mrandu ndi cimene mudzalankhula; koma ci mene cidzapatsidwa kwa inu m'mphindi yomweyo, mucilankhule; pakuti olankhula si ndinu, koma Mzimu Woyera.
12. Ndipo mbale adzapereka mbale wace kuti amuphe, ndi atate mwana wace; ndi ana adza yambana ndi akuwabala, nadzawaphetsa,
13. Ndipo adzada inu anthu onse cifukwa ca dzina langa: koma iye wakupirira kufikira cimariziro, yemweyo adzapulumutsidwa.
14. Ndipo pamene mukaona conyansa ca kupululutsa cirikuima pomwe siciyenera (wakuwerenga azindikile), pamenepo a m'Yudeya athawire kumapiri;
15. ndi iye amene ali pamwamba pa chindwi asatsike, kapena asalowe kukaturutsa kanthu m'nyumba mwace;
16. ndi iye amene ali kumunda asabwere kudzatenga Malaya ace.
17. Koma tsoka iwo akukhala ndi pakati, ndi akuyamwitsa ana masiku awol