Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Marko 13:12-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Ndipo mbale adzapereka mbale wace kuti amuphe, ndi atate mwana wace; ndi ana adza yambana ndi akuwabala, nadzawaphetsa,

13. Ndipo adzada inu anthu onse cifukwa ca dzina langa: koma iye wakupirira kufikira cimariziro, yemweyo adzapulumutsidwa.

14. Ndipo pamene mukaona conyansa ca kupululutsa cirikuima pomwe siciyenera (wakuwerenga azindikile), pamenepo a m'Yudeya athawire kumapiri;

15. ndi iye amene ali pamwamba pa chindwi asatsike, kapena asalowe kukaturutsa kanthu m'nyumba mwace;

16. ndi iye amene ali kumunda asabwere kudzatenga Malaya ace.

17. Koma tsoka iwo akukhala ndi pakati, ndi akuyamwitsa ana masiku awol

18. Ndipo pempherani kuti kusakhale m'nyengo yacisanu.

19. Pakuti masiku aja padzakhala cisautso, conga sicinakhala cinzace kuyambira ciyambi ca cilengedwe cimene Mulungu anacilenga ndi kufikira tsopano, ndipo sicidzakhalanso nthawi zonse.

20. Ndipo Ambuye akadapanda kufupikitsa masikuwo, sakadapulumuka munthu mmodzi yense; koma cifukwa ca osankhidwa amene anawasankha, anafupikitsa masikuwo.

21. Ndipo pamenepo wina akati kwa inu, Onani Kristu ali pano; kapena, Onani, uko; musabvomereze;

22. pakuti adzauka Akristu onyenga ndi aneneri onyenga, ndipo adzacita zizindikilo ndi zozizwitsa, kuti akasoceretse, ngati nkutheka, osankhidwa omwe.

23. Koma yanganirani; onani ndakuuziranitu zinthu zonse, zisanafike.

Werengani mutu wathunthu Marko 13