Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Marko 12:12-26 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Ndipo anayesa kumgwira Iye; koma anaopa khamu la anthu, pakuti anazindikira kuti Iye anakamba fanizo ili kuwatsutsa iwo; ndipo anamsiya Iye, nacoka.

13. Ndipo anatuma kwa Iye ena a Afarisi ndi a Aherode, kuti akamkole Iye m'kulankhula kwace.

14. Ndipo pamene anafika, ananena naye, Mphunzitsi, tidziwa kuti muli woona, ndipo simusamala munthu; pakuti simuyang'ana nkhope ya anthu, koma muphunzitsa njira ya Mulungu moona: Nkuloleka kodi kupereka msonkho kwa Kaisara, kapena iai?

15. Kodi tipereke kapena tisapereke? Koma Iye anadziwa cinyengo cao, nati kwa iwo, Mundiyeseranji? Nditengereni rupiya latheka, kuti ndilione. Ndipo analitenga.

16. Ndipo ananena nao, Cithunzithunzi ici, ndi cilembo cace ziri za yani? Ndipo anati kwa Iye, Za Kaisara.

17. Ndipo Yesu anati kwa iwo, Perekani zace za Kaisara kwa Kaisara, ndi zace za Mulungu kwa Mulungu. Ndipo anazizwa naye kwambiri.

18. Ndipo anadza kwa Iye Asaduki, amene amanena kuti palibe kuuka kwa akufa; ndipo anamfunsa Iye, nanena,

19. Mphunzitsi, Mose anatilembera, kuti, Akafa mbale wace wa munthu, nasiya mkazi, wosasiyapo mwana, mbale wace atenge mkazi wace, namuuldtsire mbale waceyo mbeu.

20. Analipo abale asanu ndi awiri; woyamba anakwatira mkazi, nafa, wosasiya mbeu;

21. ndipo waciwiri anamkwatira, nafa, wosasiya mbeu; ndipo wacitatunso anatero momwemo;

22. ndipo asanu ndi awiriwo analibe kusiya mbeu. Potsiriza pace pa onse mkazinso anafa.

23. Pakuuka adzakhala mkazi wa yani wa iwowa? Pakuti asanu ndi awiriwo adamuyesa mkazi wao.

24. Yesu ananena nao, Simusocera nanga mwa ici, popeza mulibe kudziwa malembo, kapena mphamvu yace ya Mulungu?

25. Pakuti pamene adzauka kwa akufa, sakwatira, kapena sakwatiwa; koma akhala ngati angelo a Kumwamba. Koma za akufa, kuti akauldtsidwa;

26. simunawerenga m'kalata wa Mose kodi, za Citsambaco, kuti Mulungu anati kwa iye, nanena, Ine Ndine Mulungu wa Abrahamu, ndi Mulungu wa Isake, ndi Mulungu wa Yakobo?

Werengani mutu wathunthu Marko 12