Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Marko 10:47-52 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

47. Ndipo pamene anamva kuti ndi Yesu wa ku Nazarete, anayamba kupfuula, ndi kunena, Yesu, Inu Mwana wa Davide, mundicitire ine cifundo.

48. Ndipo ambiri anamuyamula kuti atonthole: koma makamaka anapfuulitsa kuti, Inu Mwana wa Davide, mundicitire cifundo.

49. Ndipo Yesu anaima, nati, Mwitaneni. Ndipo anaitana wakhunguyo, nanena naye, Limba mtima; nyamuka, akuitana.

50. Ndipo iye anataya copfunda cace, nazunzuka, nadza kwa Yesu.

51. Ndipo Yesu anamyankha, nati, Ufuna kuti ndikucitire ciani? Ndipo wakhunguyo anati kwa Iye, Raboni, ndilandire kuona kwanga.

52. Ndipo Yesu anati kwa iye, Muka; cikhulupiriro cako cakupulumutsa iwe. Ndipo pomwepo anapenyanso; namtsata Iye panjira.

Werengani mutu wathunthu Marko 10