Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Marko 10:15-33 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Ndithu ndinena ndi inu, Munthu ali yense wosalandira Ufumu wa Mulungu ngati kamwana, sadzalowamo konse.

16. Ndipo Iye anatiyangata, natidalitsa, ndi kuika manja ace pa ito.

17. Ndipo pamene Iye anaturuka kutsata njira, anamthamangira munthu, namgwadira Iye, namfunsa, Mphunzitsi wabwino, ndidzacita ciani kuti ndilandire moyo wosatha?

18. Ndipo Yesu anati kwa iye, Undicha Ine wabwino bwanji? palibe wabwino koma mmodzi, ndiye Mulungu.

19. Udziwa malamulo: Usaphe, Usacite cigololo, Usabe, Usacite umboni wakunama, Usanyenge, Lemekeza atate wako ndi amako.

20. Ndipo iye anati kwa Iye, Mphunzitsi, zonsezi ndinazisunga kuyambira ndiri mwana.

21. Ndipo Yesu anamyang'ana, namkonda, nati kwa iye, Cinthu cimodzi cikusowa: pita, gulitsa zonse uli nazo, nuzipereke kwa anthu aumphawi, ndipo cuma udzakhala naco m'mwamba; ndipo ukadze kuno, unditsate Ine.

22. Koma nkhope yace inagwa pa mau awa, ndipo anacoka iye wacisoni; pakuti anali mwini cuma cambiri.

23. Ndipo Yesu anaunguzaunguza, nanena ndi ophunzira ace, Okhala naco cuma adzalowa mu Ufumu wa Mulungu ndi kubvuta nanga!

24. Ndipo ophunzirawo anazizwa ndithu ndi mau ace. Koma Yesu anayankhanso nanena nao, Ananu, nkobvuta ndithu kwa iwo akutama cuma kulowa mu Ufumu wa Mulungu!

25. Nkwa pafupi kuti ngamila ipyole diso la singano koposa kuti mwini cuma alowe mu Ufumu wa Mulungu.

26. Ndipo anadabwa, nanena kwa Iye, Ndipo angathe kupulumuka ndani?

27. Yesu anawayang'ana iwo nati, Sikutheka ndi anthu, koma kutheka ndi Mulungu; pakuti zinthu zonse zitheka ndi Mulungu.

28. Petro anayamba kunena naye, Onani, ife tinasiya zonse, ndipo tinakutsatani Inu.

29. Yesu anati, Ndinena ndi inu ndithu, Palibe munthu anasiya nyumba, kapena abale, kapena alongo, kapena amai, kapena atate, kapena ana, kapena minda, cifukwa ca Ine, ndi cifukwa ca Uthenga Wabwinowo,

30. amene sadzalandira makumi khumi tsopano nthawi yino, nyumba, ndi abale, ndi alongo, ndi amai, ndi ana, ndi minda, pamodzi ndi mazunzo; ndipo nthawi irinkudza, moyo wosatha.

31. Koma ambiri akuyamba adzakhala akuthungo, ndi akuthungo adzakhala oyamba.

32. Ndipo iwo anali m'njira alinkukwera kunka ku Yerusalemu; ndipo Yesu analikuwatsogolera; ndipo iwo anazizwa; ndipo akumtsatawo anacita mantha. Ndipo Iye anatenganso khumi ndi awiriwo, nayamba kuwauza zinthu zimene zidzamfikira Iye,

33. nati, Taonani, tikwera ku Yerusalemu; ndipo Mwana wa munthu adzaperekedwa kwa ansembe akuru ndi alembi; ndipo iwo adzamweruza kuti ayenera imfa, nadzampereka Iye kwa anthu a mitundu;

Werengani mutu wathunthu Marko 10