Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 9:9-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Ndipo anakhala masiku atatu wosaona, ndipo sanadya kapena kumwa.

10. Koma ku Damasiko kunali wophunzira wina dzina lace Hananiya; ndipo Ambuye anati kwa iye m'masomphenya, Hananiya. Ndipo anati, Ndiri pano, Ambuye,

11. Ndipo Ambuye anati kwa iye, Tauka, pita ku khwalala lochedwa Lolunjika, ndipo m'nyumba ya Yuda ufunse za munthu dzina lace Saulo, wa ku Tariso: pakuti taona, alikupemphera

12. ndipo anaona mwamuna dzina, lace Hananiya, alikulowa, namuika manja, kuti apenyenso.

13. Ndipo Hananiya anayankha nati, Ambuye ndamva ndi ambiri za munthu uyu kuti anacitiradi coipa oyera mtima anu m'Yerusalemu;

14. ndi kuti pane ali nao ulamuliro wa kwa ansembe akulu wakumanga onse akuitana pa dzina lanu.

15. Koma Ambuye anat kwa iye, Pita; pakuti iye ndiye cotengera canga cosankhika, cakunyamula dzina langa pamaso pa amitundu ndi mafumu ndi ana a Israyeli;

16. pakuti Ine ndidzamuonetsa iye zinthu zambirl ayenera iye kuzimva kuwawa cifukwaca dzina langa.

17. Ndipo anacoka Hananiya, nalowa m'nyumbayo; ndipo anaika manja ace pa iye, nati, Saulo, mbale, Ambuye wandituma ine, ndiye Yesu amene anakuonekerani pa njira wadzerayo, kuti upenyenso, ndi kudzazidwa ndi Mzimu Woyera.

18. Ndipo pomwepo padagwa kucoka m'maso mwace ngati mamba, ndipo anapenyanso;

19. ndipo ananyamuka nabatizidwa; ndipo analandira cakudya, naona naco mphamvu.Ndipo anakhala pamodzi ndi akuphunzira a ku Damasiko masiku ena.

20. Ndipo pomwepo m'masunagoge analalikira Yesu, kuti iye ndiye Mwana wa Mulungu.

21. Ndipo onse amene anamva anadabwa, nanena, Suyu iye amene anaononga m'Yerusalemu onse akuitana pa dzina ili? Ndipo wadza kuno kudzatero, kuti amuke nao omangidwa kwa ansembe akuru.

22. Koma Saulo anakula makamaka mumphamvu, nadodometsa Ayuda akukhala m'Damasiko, nawatsimikizira kuti ameneyo ndi Kristu.

23. Ndipo atapita masiku ambiri, Ayuda anapangana kuti amuphe iye;

24. koma ciwembu cao cinadziwika ndi Saulo. Ndipo anadikiranso pazipata usana ndi usiku kuti amuphe;

25. koma ophunzira ace anamtenga usiku, nampyoletsa palinga, namtsitsa ndi mtanga,

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 9