Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 8:26-31 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

26. Koma mngelo wa Ambuye analankhula ndi Filipo, nanena, Nyamuka, nupite mbali ya kumwela, kutsata njira yotsika kucokera ku Yerusalemu kunka ku Gaza; ndiyo ya cipululu.

27. Ndipo ananyamuka napita; ndipo taona munthu wa ku Aitiopiya, mdindo wamphamvu wa Kandake, mfumu yaikazi ya Aaitiopiya, ndiye wakusunga cuma cace conse, amene anadza ku Yerusalemu kudzapemphera;

28. ndipo analinkubwerera, nalikukhala pa gareta wace, nawerenga mneneri Yesaya.

29. Ndipo Mzimu anati kwa Filipo, Yandikira, nudziphatike ku gareta uyu.

30. Ndipo Filipo anamthamangira, namva iye alikuwerenga Yesaya mneneri, ndipo anati, Kodi muzindikira cimene muwerenga?

31. Koma anati, Ndingathe bwanji, popanda munthu wonditsogolera ine? ndipo anapempha Filipo akwere nakhale naye.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 8