Ndipo ananyamuka napita; ndipo taona munthu wa ku Aitiopiya, mdindo wamphamvu wa Kandake, mfumu yaikazi ya Aaitiopiya, ndiye wakusunga cuma cace conse, amene anadza ku Yerusalemu kudzapemphera;