Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 8:22-29 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

22. Cifukwa: cace lapa coipa calm ici, pemphera Ambuye, kuti kapena akukhululukire iwe colingiriraca mtima wako.

23. Pakuti ndiona kuti wagwidwa ndi ndulu yowawa ndi nsinga ya cosalungama.

24. Ndipo Simoni anayankha nati, Mundipempherere ine kwa Ambuye kuti zisandigwere izi mwanenazi.

25. Pamenepo iwo, atatha kucita umboni ndi kulankhula mau a Ambuye, anabwerakunkaku Yerusalemu, nalalikira Uthenga Wabwi no ku midzi yambirl ya Asamariya.

26. Koma mngelo wa Ambuye analankhula ndi Filipo, nanena, Nyamuka, nupite mbali ya kumwela, kutsata njira yotsika kucokera ku Yerusalemu kunka ku Gaza; ndiyo ya cipululu.

27. Ndipo ananyamuka napita; ndipo taona munthu wa ku Aitiopiya, mdindo wamphamvu wa Kandake, mfumu yaikazi ya Aaitiopiya, ndiye wakusunga cuma cace conse, amene anadza ku Yerusalemu kudzapemphera;

28. ndipo analinkubwerera, nalikukhala pa gareta wace, nawerenga mneneri Yesaya.

29. Ndipo Mzimu anati kwa Filipo, Yandikira, nudziphatike ku gareta uyu.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 8