Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 8:1-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Saulo analikubvomerezana nao pa imfa yace. Ndipo tsikulo kunayamba kuzunza kwakukuru pa Mpingo unali m'Yerusalemu; ndipo anabalalitsidwa onse m'maiko a Yudeya ndi samariya, koma osati atumwi ai.

2. Ndipo anamuika Stefano anthu opembedza, namlira maliro akuru.

3. Ndipo Saulo anapasula Mpingo, nalowa m'nyumba m'nyumba, nakokamo amuna ndi akazi, nawaika m'ndende.

4. Pamenepo ndipo iwo akubalalitsidwa anapitapita nalalikira mauwo.

5. Ndipo Filipo anatsikira ku mudzi wa ku Samarlya, nawalalikira iwo Kristu.

6. Ndipo makamuwo ndi mtima umodzi anasamalira zonenedwa ndi Filipo, pamene anamva, napenya zizindikilo zimene anazicita.

7. Pakuti ambiri a iwo akukhala nayo mizimu yonyansa inawaturukira, yopfuula ndi mau akuru; ndipo ambiri amanjenje, ndi opunduka, anaciritsidwa.

8. Ndipo panakhala cimwemwe cacikuru m'mudzimo.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 8