Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 7:5-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. ndipo sanampatsa colowa cace m'menemo, ngakhale popondapo phazi lace iai; ndipo anamlonjezera iye kuti adzampatsa ili, likhale lace, ndi la mbeu yace yomtsatira, angakhale analibe mwana pamenepo.

6. Koma Mulungu analankhula cotero, kuti mbeu yace idzakhala alendo m'dziko la eni, ndipo adzawacititsa ukapolo, nadzawacitira coipa, zaka mazana anai.

7. Ndipo mtundu amene udzawayesa akapolo, ndidzauweruza Ine, anatero Mulungu; ndipo zitapita izi adzaturuka, nadzanditumikira Ine m'malo muno.

8. Ndipo anaiupatsa iye cipangano ca mdulidwe; ndipo kotero Abrahamu anabala Isake, namdula tsiku lacisanu ndi citatu; ndi Isake anabala Yakobo, ndi Yakobo anabala makolo akulu aja khumi ndi awiri.

9. Ndipo makolo akuluwa podukidwa naye Yosefe, anamgulitsa amuke naye ku Aigupto; ndipo Mulungu anali naye,

10. namlanditsa iye m'zisautso zace zonse, nampatsa cisomo ndi nzeru pamaso pa Farao mfumu ya ku Aigupto; ndipo anamuika iye kazembe wa pa Aigupto ndi pa nyumba yace yonse.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 7