Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 7:36-53 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

36. Ameneyo anawatsogolera, naturuka nao 8 atacita zozizwa ndi zizindikilo m'Aigupto, ndi m'Nyanja Yofiira, ndi m'cipululu zaka makumi anai.

37. Uyu ndi Mose uja adati kwa ana a Israyeli, 9 Mulungu adzakuutsirani Mneneri wa mwa abale anu, monga ine.

38. 10 Uyu ndiye amene anali mu Mpingo m'cipululu pamodzi ndi mngelo wakulankhula naye m'phiri la Sina, ndi makolo athu: amene analandira maneno amoyo akutipatsa ife;

39. amene makolo athu sanafuna kumvera iye, koma anamkankha acoke, nabwerera m'mbuyo mumtima mwao ku Aigupto,

40. 11 nati ndi Aroni, Tipangireni milungu yotitsogoleraife; pakuti Mose uja, amene anatiturutsa m'Aigupto, sitidziwa comwe camgwera.

41. Ndipo 12 anapanga mwana wa ng'ombe masiku omwewo, nabwera nayo nsembe kwa fanolo, nasekerera ndi nchito za manja ao.

42. Koma 13 Mulungu anatembenuka, nawapereka iwo atumikire gulu la kumwamba; monga kwalembedwa m'buku laaneneri,14 Kodi mwapereka kwa Ine nyama zophedwa ndi nsembeZaka makumi anai m'cipululu, nyumba ya Israyeli inu?

43. 15 Ndipo munatenga cihema ca Moloki,Ndi nyenyezi ya mulungu Refani,Zithunzizo mudazipanga kuzilambira;Ndipo ndidzakutengani kunka nanu m'tsogolo mwace mwa Babulo.

44. Cihema ca umboni cinali ndi makolo athu m'cipululu, monga adalamula iye wakulankhula ndi Mose, 16 acipange ici monga mwa cithunzico adaciona.

45. 17 Cimenenso makolo athu akudza m'mbuyo, analowa naco ndi Y oswa polandira iwo zao za amitundu, 18 amene Mulungu anawaingitsa pamaso pa makolo athu, kufikira masiku a Davine;

46. amene anapeza cisomo pamaso pa Mulungu, napempha kuti apeze mokhalama Mulungu wa Yakobo.

47. Kama 19 Solomo anammangira nyumba.

48. Komatu 20 Wamwambamwambayo sakhala m'nyumba zomangidwa ndi manja; monga mneneri anena,

49. 21 Thambo la kumwamba ndilo mpando wacifumu wanga,Ndi dziko lapansi copondapo mapazi anga:Mudzandimangira nyumba yotani? ati Ambuye;Kapena malo a mpumulo wanga ndi otani?

50. Silinapanga dzanja langa zinthu izi zonse kodi?

51. 22 Ouma khosi ndi osadulidwa mtima ndi makutu inu, mukaniza Mzimu Woyera nthawi zonse; monga anacita makolo anu, momwemo inu.

52. 23 ndiye yani wa aneneri makolo anu sanamzunza? ndipo anawapha iwo amene anaonetseratu za kudzakwace kwa Wolungamayo; wa iye amene mwakhala tsopano akumpereka ndi akumupha;

53. inu amene munalandira cilamulo 24 monga cidaikidwa ndi angelo, ndipo simunacisunga.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 7