35. Mose uyu amene anamkana, ndi kuti, Wakuika iwe ndani mkuru ndi woweruza? ameneyo Mulungu anamtuma akhale mkuru, ndi mombolo, ndi dzanja la mngelo womuonekera pacitsamba.
36. Ameneyo anawatsogolera, naturuka nao 8 atacita zozizwa ndi zizindikilo m'Aigupto, ndi m'Nyanja Yofiira, ndi m'cipululu zaka makumi anai.
37. Uyu ndi Mose uja adati kwa ana a Israyeli, 9 Mulungu adzakuutsirani Mneneri wa mwa abale anu, monga ine.
38. 10 Uyu ndiye amene anali mu Mpingo m'cipululu pamodzi ndi mngelo wakulankhula naye m'phiri la Sina, ndi makolo athu: amene analandira maneno amoyo akutipatsa ife;
39. amene makolo athu sanafuna kumvera iye, koma anamkankha acoke, nabwerera m'mbuyo mumtima mwao ku Aigupto,
40. 11 nati ndi Aroni, Tipangireni milungu yotitsogoleraife; pakuti Mose uja, amene anatiturutsa m'Aigupto, sitidziwa comwe camgwera.