Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 7:34-44 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

34. 7 Kuona ndaona coipidwa naco anthu anga ali m'Aigupto, ndipo a amva kubuula kwao; ndipo ndatsika kuwalanditsa; ndipo tsopano tiye kuno, ndikutume ku Aigupto

35. Mose uyu amene anamkana, ndi kuti, Wakuika iwe ndani mkuru ndi woweruza? ameneyo Mulungu anamtuma akhale mkuru, ndi mombolo, ndi dzanja la mngelo womuonekera pacitsamba.

36. Ameneyo anawatsogolera, naturuka nao 8 atacita zozizwa ndi zizindikilo m'Aigupto, ndi m'Nyanja Yofiira, ndi m'cipululu zaka makumi anai.

37. Uyu ndi Mose uja adati kwa ana a Israyeli, 9 Mulungu adzakuutsirani Mneneri wa mwa abale anu, monga ine.

38. 10 Uyu ndiye amene anali mu Mpingo m'cipululu pamodzi ndi mngelo wakulankhula naye m'phiri la Sina, ndi makolo athu: amene analandira maneno amoyo akutipatsa ife;

39. amene makolo athu sanafuna kumvera iye, koma anamkankha acoke, nabwerera m'mbuyo mumtima mwao ku Aigupto,

40. 11 nati ndi Aroni, Tipangireni milungu yotitsogoleraife; pakuti Mose uja, amene anatiturutsa m'Aigupto, sitidziwa comwe camgwera.

41. Ndipo 12 anapanga mwana wa ng'ombe masiku omwewo, nabwera nayo nsembe kwa fanolo, nasekerera ndi nchito za manja ao.

42. Koma 13 Mulungu anatembenuka, nawapereka iwo atumikire gulu la kumwamba; monga kwalembedwa m'buku laaneneri,14 Kodi mwapereka kwa Ine nyama zophedwa ndi nsembeZaka makumi anai m'cipululu, nyumba ya Israyeli inu?

43. 15 Ndipo munatenga cihema ca Moloki,Ndi nyenyezi ya mulungu Refani,Zithunzizo mudazipanga kuzilambira;Ndipo ndidzakutengani kunka nanu m'tsogolo mwace mwa Babulo.

44. Cihema ca umboni cinali ndi makolo athu m'cipululu, monga adalamula iye wakulankhula ndi Mose, 16 acipange ici monga mwa cithunzico adaciona.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 7