Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 7:3-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. nati kwa iye, Turuka ku dziko lako ndi kwa abale ako, ndipo tiye ku dziko limene ndidzakusonyeza iwe.

4. Pamenepo anaturuka m'dziko la Akaldayo namanga m'Harana: ndipo, kucokera kumeneko, atamwalira atate wace, Mulungu anamsuntha alowe m'dziko lino, m'mene mukhalamo tsopano;

5. ndipo sanampatsa colowa cace m'menemo, ngakhale popondapo phazi lace iai; ndipo anamlonjezera iye kuti adzampatsa ili, likhale lace, ndi la mbeu yace yomtsatira, angakhale analibe mwana pamenepo.

6. Koma Mulungu analankhula cotero, kuti mbeu yace idzakhala alendo m'dziko la eni, ndipo adzawacititsa ukapolo, nadzawacitira coipa, zaka mazana anai.

7. Ndipo mtundu amene udzawayesa akapolo, ndidzauweruza Ine, anatero Mulungu; ndipo zitapita izi adzaturuka, nadzanditumikira Ine m'malo muno.

8. Ndipo anaiupatsa iye cipangano ca mdulidwe; ndipo kotero Abrahamu anabala Isake, namdula tsiku lacisanu ndi citatu; ndi Isake anabala Yakobo, ndi Yakobo anabala makolo akulu aja khumi ndi awiri.

9. Ndipo makolo akuluwa podukidwa naye Yosefe, anamgulitsa amuke naye ku Aigupto; ndipo Mulungu anali naye,

10. namlanditsa iye m'zisautso zace zonse, nampatsa cisomo ndi nzeru pamaso pa Farao mfumu ya ku Aigupto; ndipo anamuika iye kazembe wa pa Aigupto ndi pa nyumba yace yonse.

11. Koma inadza njala pa Aigupto ndi Kanani lonse, ndi cisautso cacikuru; ndipo sanapeza cakudya makolo athu.

12. Koma pakumva Yakobo kuti muli tirigu m'Aigupto, anatuma makolo athu ulendo woyamba,

13. Ndipo pa ulendo waciwiri Y osefe anazindikirika ndi abale ace; ndipo pfuko la Yosefe linaonekera kwa Farao.

14. Ndipo Yosefe anatumiza, naitana Yakobo atate wace, ndi a banja lace lonse, ndiwo anthu makumi asanu ndi awiri mphambu asanu.

15. Ndipo Yakobo anatsikira ku Aigupto; ndipo anamwalira, iye ndi makolo athu;

16. ndipo anawanyamula kupita nao ku Sukemu, nawaika m'manda amene Abrahamu adagula ndi mtengo wace wa ndalama kwa ana a Emori m'Sukemu.

17. Koma m'mene inayandikira nthawi ya lonjezo limene Mulungu adalonjezana ndi Abrahamu, anthuwo anakula nacuruka m'Aigupto,

18. kufikira inauka mfumu yina pa Aigupto, imene siinamdziwa Yosefe.

19. Imeneyo inacenjerera pfuko lathu, niwacitira coipa makolo athu, niwatayitsa tiana tao, kuti tingakhale ndi moyo.

20. Nyengo yomweyo anabadwa Mose, ndiye wokoma ndithu; ndipo anamlera miyezi itatu m'nyumba ya atate wace:

21. ndipo pakutayika iye, anamtola mwana wamkazi wa Farao, namlera akhale mwana wace.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 7