Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 7:29-38 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

29. 2 Ndipo Mose anathawa pa mau awa, nakhala mlendo m'dziko la Midyani; kumeneko anabala ana amuna awiri.

30. Ndipo 3 zitapita zaka makumi anai, anamuonekera mngelo m'cipululu ca Sina, m'lawi la mota wa m'citsamba.

31. 4 Koma Mose pakuona, anazizwa pa coonekaco; ndipo pakuyandikira iye kukaona, kunadza mau a Ambuye,

32. 5 akuti, Ine ndine Mulungu wa makolo anu, Mulungu wa Abrahamu, ndi wa Isake, ndi wa Yakobo. Ndipo Mose ananthunthumira, osalimbika mtima kupenyetsako.

33. 6 Ndipo Ambuye anati kwa iye, Masula nsapato ku mapazi ako; pakuti pa malo amene upondapo mpopatulika.

34. 7 Kuona ndaona coipidwa naco anthu anga ali m'Aigupto, ndipo a amva kubuula kwao; ndipo ndatsika kuwalanditsa; ndipo tsopano tiye kuno, ndikutume ku Aigupto

35. Mose uyu amene anamkana, ndi kuti, Wakuika iwe ndani mkuru ndi woweruza? ameneyo Mulungu anamtuma akhale mkuru, ndi mombolo, ndi dzanja la mngelo womuonekera pacitsamba.

36. Ameneyo anawatsogolera, naturuka nao 8 atacita zozizwa ndi zizindikilo m'Aigupto, ndi m'Nyanja Yofiira, ndi m'cipululu zaka makumi anai.

37. Uyu ndi Mose uja adati kwa ana a Israyeli, 9 Mulungu adzakuutsirani Mneneri wa mwa abale anu, monga ine.

38. 10 Uyu ndiye amene anali mu Mpingo m'cipululu pamodzi ndi mngelo wakulankhula naye m'phiri la Sina, ndi makolo athu: amene analandira maneno amoyo akutipatsa ife;

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 7