Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 7:2-5 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Ndipo Stefano anati, Amuna inu, abale, ndi atate, tamverani. Mulungu wa ulemerero anaonekera kwa kholo lathu Abrahamu, pokhala iye m'Mesopotamiya, asanayambe kukhala m'Harana;

3. nati kwa iye, Turuka ku dziko lako ndi kwa abale ako, ndipo tiye ku dziko limene ndidzakusonyeza iwe.

4. Pamenepo anaturuka m'dziko la Akaldayo namanga m'Harana: ndipo, kucokera kumeneko, atamwalira atate wace, Mulungu anamsuntha alowe m'dziko lino, m'mene mukhalamo tsopano;

5. ndipo sanampatsa colowa cace m'menemo, ngakhale popondapo phazi lace iai; ndipo anamlonjezera iye kuti adzampatsa ili, likhale lace, ndi la mbeu yace yomtsatira, angakhale analibe mwana pamenepo.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 7