Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 7:1-5 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo mkulu wa ansembe anati, Zitero izi kodi?

2. Ndipo Stefano anati, Amuna inu, abale, ndi atate, tamverani. Mulungu wa ulemerero anaonekera kwa kholo lathu Abrahamu, pokhala iye m'Mesopotamiya, asanayambe kukhala m'Harana;

3. nati kwa iye, Turuka ku dziko lako ndi kwa abale ako, ndipo tiye ku dziko limene ndidzakusonyeza iwe.

4. Pamenepo anaturuka m'dziko la Akaldayo namanga m'Harana: ndipo, kucokera kumeneko, atamwalira atate wace, Mulungu anamsuntha alowe m'dziko lino, m'mene mukhalamo tsopano;

5. ndipo sanampatsa colowa cace m'menemo, ngakhale popondapo phazi lace iai; ndipo anamlonjezera iye kuti adzampatsa ili, likhale lace, ndi la mbeu yace yomtsatira, angakhale analibe mwana pamenepo.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 7