Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 6:10-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Ndipo sanathe kuilaka nzeru ndi Mzimu amene analankhula naye.

11. Pamenepo anafuna anthu akumpitira pansi, ndi kuti, Tidamumva iye alikunenera Mose ndi Mulungu mau amwano.

12. Ndipo anautsa anthu, ndi akuru, ndi alembi, namfikira, namgwira iye, nadza naye ku bwalo la akulu,

13. naimika mboni zonama, zakunena, Munthu ameneyo saleka kunenera malo oyera amene, ndi cilamulo;

14. pakuu tinamumva iye alikunena, kuti, Yesu Mnazarayo amene adzaononga malo ano, nadzasanduliza miyambo imene Mose anatipatsa.

15. Ndipo anampenyetsetsa onse akukhala m'bwalo la akulu, naona nkhope yace ngati nkhope ya mnaelo.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 6