Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 4:16-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. kuti, Tidzawacitira ciani anthu awa? pakutitu caoneka kwa onse akukhala m'Yerusalemu kuti cizindikilo cozindikirika cacitidwa ndi iwo, ndipo sitingathe kukana.

17. Komatu tiwaopse asalankhulenso m'dzina ili kwa munthu ali yense, kuti cisabukenso kwa anthu.

18. Ndipo anawaitana, nawalamulira kuti asanene konse kapena kuphunzitsa m'dzina la Yesu.

19. Koma Petro ndi Yohane anayankha nati kwa iwo, Weruzani, ngati nkwabwino pamaso pa Mulungu kumvera inu koposa Mulungu;

20. pakuti sitingatheife kuleka kulankhula zimene tinaziona ndi kuzimva.

21. Koma m'mene anawaopsanso anawamasula, osapeza kanthu kakuwalanga, cifukwa ca anthu; pakuti onse analemekeza Mulungu cifukwa ca comwe cidacitika.

22. Pakuti anali wa zaka zace zoposa makumi anai munthuyo, amene cizindikilo ici cakumciritsa cidacitidwa kwa iye.

23. Ndipo m'mene anamasulidwa, anadza kwa anzao a iwo okha, nawauza ziri zonse oweruza ndi akulu adanena nao.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 4