Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 4:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Koma m'mene analikulankhula ndi anthu, ansembe ndi mdindo wa kuKacisi ndi Asaduki anadzako,

2. obvutika mtima cifukwa anaphunzitsa anthuwo, nalalikira mwa Yesu kuuka kwa akufa.

3. Ndipo anawathira manja, nawaika m'ndende kufikira m'mawa; pakuti mpa madzulo pamenepo.

4. Koma ambiri a iwo amene adamva mau anakhulupira; ndipo ciwerengero ca amuna cinali ngati zikwi zisanu.

5. Koma panali m'mawa mwace, anasonkhana pamodzi m'Yerusalemu oweruza, ndi akulu, ndi alembi;

6. ndi Anasi mkulu wa ansembe, ndi Kayafa, ndi Yohane, ndi Alesandro, ndi onse amene anali a pfuko la mkulu waansembe.

7. Ndipo m'mene anawaimika pakati, anafunsa kuti, Ndi mphamvu yanji, kapena m'dzina lanji, mwacita ici inu?

8. Pamenepo Petro, wodzala ndi Mzimu Woyera anati kwa iwo, Oweruza a anthu inu, ndi akulu,

9. ngati ife lero tiweruzidwa cifukwa ca nchito yabwino ya pa munthu wodwala, ndi maciritsidwe ace,

10. zindikirani inu nonse, ndi anthu onse a Israyeli, kuti m'dzina la Yesu Kristu Mnazarayo, amene inu munampacika pamtanda, amene Mulungu anamuukitsa kwa akufa, mwa Iyeyu munthuyu aimirirapo pamaso panu, wamoyo.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 4