Koma pamene akunjawo anaona ciromboco ciri lende pa dzanja lace, ananena wina ndi mnzace, Zoona munthuyu ndiye wambanda, angakhale anapulumuka m'nyanja, cilungamo sicimlola akhale ndi moyo.