Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 28:1-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo titapulumuka, pamenepo tinadziwa kuti cisumbuco cinachedwa Melita.

2. Ndipo akunja anaticitira zokoma zosacitika pena ponsepo; pakuti anasonkha moto, natilandira ife tonse, cifukwa ca mvula inalinkugwa, ndi cifukwa ca cisanu.

3. Koma pamene Paulo adaola cisakata ca nkhuni, naciika pamoto, inaturukamo njoka, cifukwa ca kutenthaku, nilumadzanja lace.

4. Koma pamene akunjawo anaona ciromboco ciri lende pa dzanja lace, ananena wina ndi mnzace, Zoona munthuyu ndiye wambanda, angakhale anapulumuka m'nyanja, cilungamo sicimlola akhale ndi moyo.

5. Koma anakutumulira ciromboco kumoto, osamva kupweteka.

6. Koma anayesa kuti adzatupa, kapena mwini wace kugwa kufa pomwepo; koma m'mene adalindira nthawitu, naona kuti sikunampweteka, anapindula, nati, Ndiye Mulungu.

7. Koma pafupt pamenepo panali minda, mwini wace ndiye mkulu cisumbuco, dzina lace Popliyo; amene anatilandira ife, naticereza okoma masiku atatu.

8. Ndipo kunatero kuti atate wace wa Popliyo anagona wodwala nthenda ya malungo ndi kamwazi. Kwa iyeyu Paulo analowa, napemphera, naika manja pa iye, namciritsa.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 28