Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 28:21-28 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

21. Ndipo anati kwa iye, Ife sitinalandira akalata onena za inu ocokera ku Yudeya, kapena sanadza kuno wina wa abale ndi kutiuza kapena kulankhula kanthu koipa ka inu.

22. Koma tifuna kumva mutiuze muganiza ciani; pakuti za mpatuko uwu, tidziwa kuti aunenera ponse ponse.

23. Ndipo pamene adampangira tsiku, anadza ku nyumba yace anthu ambiri; amenewo anawafotokozera, ndikucitira umboni Ufumu wa Mulungu, ndi kuwakopa za Yesu, zocokera m'cilamulo ca Mose ndi mwa aneneri, kuyambira mamawa kufikira madzulo.

24. Ndipo ena anamvera zonenedwazo, koma ena sanamvera.

25. Koma popeza sanabvomerezana, anacoka atanena Paulo mau amodzi, kuti, Mzimu Woyera analankhula kokoma mwa Yesaya Mneneri kwa makolo anu,

26. ndi kuti,Pita kwa anthu awa, nuti,Ndi kumva mudzamva, ndipo simudzazindikira konse;Ndipo pakupenya mudzapenya, koma osaona konse;

27. Pakuti mtima wa anthu awa watupatu,Ndipo m'makutu mwao mmolemakumva,Ndipo masoao anawatseka;Kuti angaone ndi maso,Nangamve ndi makutu,Nangazindikire ndi mtima,Nangatembenuke,Ndipo Ine ndingawaciritse.

28. Potero, dziwani inu, kuti cipulumutso ici ca Mulungu citumidwa kwa amitundu; iwonsoadzamva. [

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 28