Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 28:16-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Ndipo pamene tinalowa m'Roma, analola Paulo akhale pa yekha ndi msilikari womdikira iye.

17. Ndipo kunali, atapita masiku atatu, anaitana akulu a Ayuda asonkhane; ndipo atasonkhana, ananena nao, Ine, amuna, abale, ndingakhale sindinacita kanthu kakuipsa anthu, kapena miyambo ya makolo, anandipereka wam'nsinga kucokera ku Yerusalemu ku manja a Aroma;

18. ndiwo, atandifunsafunsa ine anafuna kundimasula, popeza panalibe cifukwa ca kundiphera.

19. Koma pakukanapo Ayuda, ndinafulumidwa mtima kuturukira kwa Kaisara; si kunena kuti ndinali nako kanthu kakunenera mtundu wanga.

20. Cifukwa ca ici tsono ndinakupemphani inu mundione ndi kulankhula nane; pakuti cifukwa ca ciyembekezo ca Israyeli ndamangidwa ndi unyolo uwu.

21. Ndipo anati kwa iye, Ife sitinalandira akalata onena za inu ocokera ku Yudeya, kapena sanadza kuno wina wa abale ndi kutiuza kapena kulankhula kanthu koipa ka inu.

22. Koma tifuna kumva mutiuze muganiza ciani; pakuti za mpatuko uwu, tidziwa kuti aunenera ponse ponse.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 28