Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 27:35-44 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

35. Ndipo atanena izi, ndi kutenga mkate, anayamika Mulungu pamaso pa onse; ndipo m'mene adaunyema anayamba kudya.

36. Ndipo anakhala olimbika mtima onse, natenga cakudya iwo omwe.

37. Ndipo life tonse tiri m'ngalawa ndife anthu mazana awiri mphambu makumi asanu ndi awiri kudza asanu ndi mmodzi.

38. Ndipo m'mene anakhuta, anapepuza ngalawa, nataya tirigu m'nyarija.

39. Ndipo kutaca sanazindikira dzikolo; koma anaona pali bondo la mcenga; kumeneko anafuna, ngati nkutheka, kuyendetsako ngalawa.

40. Ndipo m'mene anataya anangula anawasiya m'nyanja, namasulanso zingwe zomanga tsigiro; ndipo pokweza thanga la kulikuru, analunjikitsa kumcenga.

41. Koma pofika pamalo pokomana mafunde awiri, anatsamitsapo ngalawa; ndipo kulikuru kunatsama, ndi kukhala kosasunthika, koma kumakaliro kunasweka ndi mphamvu ya mafunde.

42. Ndipo uphungu wa asilikari udati awapheandende, angasambire, ndi kuthawa.

43. Koma kenturiyo, pofuna kupulumutsa Paulo, anawaletsa angacite ca uphungu wao; nalamula kuti iwo akukhoza kusambira ayambe kudziporiya m'nyanja, nafike pamtunda,

44. ndipo otsalawo, ena pamatabwa, ndi ena pa zina za m'ngalawa. Ndipo kudatero kuti lonse adapulumukira pamtunda.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 27