Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 27:22-32 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

22. Koma tsopano ndikucenjezani mulimbike mtima; pakuti sadzatayika wamoyo mmodzi mwa inu, koma ngalawa ndiyo.

23. Pakuti anaimirira kwa ine usiku walero mngelo wa Mulungu amene ndiri wace, amenenso ndimtumikira,

24. nanena, Usaope Paulo; ukaimirira pamaso pa Kaisara; ndipo, taona, Mulungu anakupatsa onse amene akuyenda nawe pamodzi.

25. Cifukwa cace, limbikani mtima, amuna inu; pakuti ndikhulupirira Mulungu, kuti kudzatero monga momwe ananena ndi ine.

26. Koma tiyenera kutayika pa cisumbu cakuti.

27. Koma pofika usiku wakhumi ndi cinai, potengedwa ife kwina ndi kwina m'nyanja ya Adriya, pakati pa usiku amarinyero anazindikira kuti analikuyandikira kumtunda;

28. ndipo anayesa madzi, napeza mikwamba makumi awiri; ndipo katapita kanthawi, anayesanso, napeza mikwamba khumi ndi isanu.

29. Ndipo pakuopa tingatayike pamiyala, anaponya anangula anai kumakaliro, nakhumba kuti kuce.

30. Ndipo m'mene amarinyero anafunakuthawa m'ngalawa, natsitsira bwato m'nyanja, monga ngati anati aponye anangula kulikuru,

31. Paulo anati kwa kenturiyo ndi kwa asilikari, Ngati awa sakhala m'ngalawa inu simukhoza kupulumuka.

32. Pamenepo asilikari anadula zingwe za bwato, naligwetsa.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 27