Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 27:20-34 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

20. Ndipo m'mene dzuwa kapena nyenyezi sizinatiwalira masiku ambiri, ndipo namondwe wosati wamng'ono anatigwera, ciyembekezo conse cakuti tipulumuke cidaticokera pomwepo.

21. Ndipo pamene atakhala nthawi yaikuru osadya kanthu, Paulo anaimirira pakati pao, nati, Amuna inu, mukadamvera ine, osacoka ku Krete, osadzitengera kuonongeka ndi kutayika kumene.

22. Koma tsopano ndikucenjezani mulimbike mtima; pakuti sadzatayika wamoyo mmodzi mwa inu, koma ngalawa ndiyo.

23. Pakuti anaimirira kwa ine usiku walero mngelo wa Mulungu amene ndiri wace, amenenso ndimtumikira,

24. nanena, Usaope Paulo; ukaimirira pamaso pa Kaisara; ndipo, taona, Mulungu anakupatsa onse amene akuyenda nawe pamodzi.

25. Cifukwa cace, limbikani mtima, amuna inu; pakuti ndikhulupirira Mulungu, kuti kudzatero monga momwe ananena ndi ine.

26. Koma tiyenera kutayika pa cisumbu cakuti.

27. Koma pofika usiku wakhumi ndi cinai, potengedwa ife kwina ndi kwina m'nyanja ya Adriya, pakati pa usiku amarinyero anazindikira kuti analikuyandikira kumtunda;

28. ndipo anayesa madzi, napeza mikwamba makumi awiri; ndipo katapita kanthawi, anayesanso, napeza mikwamba khumi ndi isanu.

29. Ndipo pakuopa tingatayike pamiyala, anaponya anangula anai kumakaliro, nakhumba kuti kuce.

30. Ndipo m'mene amarinyero anafunakuthawa m'ngalawa, natsitsira bwato m'nyanja, monga ngati anati aponye anangula kulikuru,

31. Paulo anati kwa kenturiyo ndi kwa asilikari, Ngati awa sakhala m'ngalawa inu simukhoza kupulumuka.

32. Pamenepo asilikari anadula zingwe za bwato, naligwetsa.

33. Ndipo popeza kulinkuca, Paulo anawacenjeza onse adye kanthu, nati, Lero ndilo tsiku lakhumi ndi cinai limene munalindira, ndi kusala cakudya, osalawa kanthu.

34. Momwemo ndikucenjezani mutenge kanthu kakudya; pakuti kumeneku ndi kwa cipulumutsocanu; pakuti silidzatayika tsitsi la pa mutu wa mmodzi wa inu.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 27