Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 26:14-26 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Ndipo pamene tidagwa pansi tonse, ndinamva mau akunena kwa ine m'cinenedwe ca Cihebri, Saulo, Saulo, undilondalonderanji Ine? nkukubvuta kutsalima pacothwikira.

15. Ndipo ndinati, Ndinu yani Mbuye? Ndipo Ambuye anati, Ine ndine Yesu amene iwe umlondalonda.

16. Komatu uka, imirira pa mapazi ako; pakuti cifukwa ca ici ndinaonekera kwa iwe, kukuika iwe ukhale mtumiki ndi mboni ya izi wandionamo Ine, ndiponso ya izi ndidzakuonekeramo we;

17. ndi kukulanditsa kwa anthu, ndi kwa amitundu, amene Ine ndikutuma kwa iwo,

18. kukawatsegulira maso ao, kuti atembenuke kucokera kumdima, kulinga kukuunika, ndi kucokera ulamuliro wa Satana kulinga kwa Mulungu, kuti alandire iwo cikhululukiro ca macimo, ndi colowa mwa iwo akuyeretsedwa ndi cikhulupiriro ca mwa Ine.

19. Potero, Mfumu Agripa, sindinakhala ine wosamvera masomphenya a Kumwamba;

20. komatu kuyambira kwa iwo a m'Damasiko, ndi a m'Yerusalemu, ndi m'dziko lonse la Yudeya, ndi kwa amitundunso ndinalalikira kuti alape, natembenukire kwa Mulungu, ndi kucita nchito zoyenera kutembenuka mtima.

21. Cifukwa ca izi Ayuda anandigwira m'Kacisi, nayesa kundipha.

22. Pamenepo pothandizidwa ndi Mulungu, ndiimirira kufikira lero lino, ndi kuwacitira umboni ang'ono ndi akuru, posanena kanthu kena koma zimene aneneri ndi Mose ananenazidzafika;

23. kuti Kristu akamve zowawa, kuti iye, woyamba mwa kuuka kwa akufa, adzalalikira kuunika kwa anthu ndi kwa amitundu.

24. Koma pakudzikanira momwemo, Festo anati ndi mau akuru, Uli wamisala Paulo; kuwerengetsa kwako kwakucititsa misala.

25. Koma Paulo anati, Ndiribe misala, Festo womvekatu; koma nditurutsa mau a coonadi ndi odziletsa.

26. Pakuti mfumuyo idziwa izi, kwa iye imene ndilankhula nayonso mosaopa: pakuti ndidziwadi kuti kulibe kanthu ka izi kadambisikira; pakuti ici Sicinacitika m'tseri.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 26